Posts

Showing posts from July, 2024

UBWINO WA ULIMI WA NSOMBA KWA ALIMI NDI KWA OGWIRA NTCHITO: NKHANI YA DAMU LA DR. NAPOLEON DZOMBE KU DOWA MFUMU YAYIKULU KAYEMBE

Image
  Kuweta somba ndi mbali imodzi ya ulimi ofunikira kwambiri pa chitukuko cha alimi ndi dziko lonse la Malawi. Ulimiwu umachitika kwambiri mmadera amene madzi amapezeka mosavuta monga mmbali mwa mitsinje, nyanja komaso Madera amene madzi amasungika bwino nthawi yamvula ndiyadzuwa yomwe. Maboma monga; Salima, Mangochi, Nkhataby ndi ena ambali mwa nyanja amakhala ndkuthekera kochuluka kochita ulimiwu chifukwa nkhani yamadzi kwa Iwo sivuto. Ulimi wamitsinje ing'onoing'ono umafuna ntchito yochuluka maka potseka njira imene madzi amayendamo. Ndipo ulimi oterewu ukuchitika kwambiri mmadera akumtunda monga Dowa, Lilongwe ndi Kasungu mchigawo chapakati omwe alikutali ndi nyanja ya Malawi. Damu limene a Dr. Napoleon Dzombe akupangapo ulimi wasomba. Tinayenda mboma la Dowa kwa Mkanire dera la fumu yayikulu Kayembe komwe kukuchitika zitukuko zosiyanasiyana mogwiriza ndimasomphenya a Malawi 2063 monga: zokopa alendo, ulimi wa mthilira komaso ulimi wasomba motsogozedwa ndi Dr. Napoleon Dzomb...