UBWINO WA ULIMI WA NSOMBA KWA ALIMI NDI KWA OGWIRA NTCHITO: NKHANI YA DAMU LA DR. NAPOLEON DZOMBE KU DOWA MFUMU YAYIKULU KAYEMBE
Kuweta somba ndi mbali imodzi ya ulimi ofunikira kwambiri pa chitukuko cha alimi ndi dziko lonse la Malawi. Ulimiwu umachitika kwambiri mmadera amene madzi amapezeka mosavuta monga mmbali mwa mitsinje, nyanja komaso Madera amene madzi amasungika bwino nthawi yamvula ndiyadzuwa yomwe. Maboma monga; Salima, Mangochi, Nkhataby ndi ena ambali mwa nyanja amakhala ndkuthekera kochuluka kochita ulimiwu chifukwa nkhani yamadzi kwa Iwo sivuto. Ulimi wamitsinje ing'onoing'ono umafuna ntchito yochuluka maka potseka njira imene madzi amayendamo. Ndipo ulimi oterewu ukuchitika kwambiri mmadera akumtunda monga Dowa, Lilongwe ndi Kasungu mchigawo chapakati omwe alikutali ndi nyanja ya Malawi.
Damu limene a Dr. Napoleon Dzombe akupangapo ulimi wasomba.
Tinayenda mboma la Dowa kwa Mkanire dera la fumu yayikulu Kayembe komwe kukuchitika zitukuko zosiyanasiyana mogwiriza ndimasomphenya a Malawi 2063 monga: zokopa alendo, ulimi wa mthilira komaso ulimi wasomba motsogozedwa ndi Dr. Napoleon Dzombe. Iwowa anapanga Damu mdera lawo lomwe limathandizira ntchito zaulimi wasomba, zokopa alendo komaso ulimi wa mthilirawu. Ntchito yokumba damuli anayayiyamba mchaka cha 2009 kufika pano mu 2024 akwanitsa kukumba malo otalika pafupifupi 1 kilomita zomwe zikupangitsa kuti lizikwanitsa kugwira ntchito zosiyanasiyana chifukwa chakuchuluka kwa madzi mdamuli.
Titafika pamalo pomwe pali damuli, tinacheza ndi asodzi asomba omwe akhala akugwira ntchito kwazaka zinayi tsopano. Anatifotokozera zokhudza mitundu ya somba zomwe zikupezeka mdamuli monga, Chambo, Milamba, Matemba komaso Micheni kungotchulapo yochepa. "Milamba ndi mtundu umodzi wasomba umene zikumakula kwambiri mpaka kufika makilogiramu asanu ndi atatu umodzi" mmodzi mwa asodzi anayankhula. Anati pa tsiku lililonse amakwanitsa kupha nsomba zokwanira makilogiramu osachepera khumi ndi asanu. Pamakilogiramu osewa theka limakhala la Milamba yomwe imagulitsidwa pa mtengo wapafupifupi K6,000 pa kilogiramu iliyonse.
Matemba: wina mwa mtundu wasomba zikupezeka mudamuli.
Anapitiliza kufotokoza ubwino umene iwo akupeza ngati antchito komaso a Dr. Napoleon Dzombe omwe akupanga ulimiwu. "Ife ngati antchito tikupindula kwambiri, pa ntchito imeneyi timalandira ndalama mwezi ukatha komaso nsomba zina amatha kutigawira zomwe zimatithandizira moyo wathu watsikunditsiku kupeza chakudya komaso kugula zosowa zathu" asodziwa anayankhula. " Dr. Napoleon Dzombe ngati eniake a ntchito yonseyi akupindula kwambiri, kutengera ndalama zimene timagulitsa tsiku ndi tsiku motsogozedwa ndi a sekilitale sizimachepera K40,000 zimene zikutanthauza kuti pakutha pa mwezi amapanga ndalama kupitilira K1,200,000." Kupatula ndalama zimene amapeza, anatiso damuli limathandiza pa ulimi wa nthochi umene a Dr. Napoleon Dzombe amalima komaso ntchito zokopa alendo amene amabwera kudzawona damuli.
Mavuto omwe akukumana nawo ngati ogwira ntchito ndimonga kusowa kwazipangizo zophera mitundu ina ya somba monga Matemba komaso Micheni zomwe zikupangitsa kuti asamaphe somba zochuluka monga mmene zimafunikira. Vuto lina ndinyengo yachisanu imene imasokozeka kaphedwe kasomba. Mwachitsanzo munyengo yotentha amakwanitsa kupha nsomba zoposera makilogiramu makumi asanu pamene miyezi ngati May, June ndi July akungokwanitsa makilogiramu makumi atatu kukalekeza makumi anayi okha. Izi zimachitika chifukwa nthawiyi nsomba zimayenda pansi kwambiri kuthawa kunzinzira zomwe zimapangitsa kuti azivutika kuzipha chifukwa chakutalika kwake kwa damuli.
Zina mwa galimoto zogwiritsa ntchito pokumba Damu.
Kwa alimi ang'onoang'ono kumakhala kovuta kuti akwanitse zimene Dr. Napoleon Dzombe akupanga chifukwa chakuchepekedwa kwandalama zoti angagwiritse ntchito pokumba Damu lawo ndi kulipira antchito komaso kugula zipangizo zogwiritsa ntchito. Vuto lina limene amakumana nalo kuti ayambe ulimiwu ndikusowa kwamalo okwanira woti akhoza kukozapo Damu. Pamavuto onsewa ndizotheka kuthana nawo; mwachitsazo alimi akhoza kukhala mmagulu ndikumachitira zinthu pamodzi ndikuchepetsa ndalama zimene angasonkhe kuyekeza ndi kuchita izi payekha. Alimi ena amuderali amene amafunitsitsa atachita ulimiwu, anatiuza akupanga chiganizo chopanga zinthu pamodzi ndi alimi azawo maka amene ayandikira kwambiri ndi mitsinje kuti akhoza kupanga Damu kuti ayambe ulimiwu.
Ulimi wasomba ku Malawi kuno ukuthandizira mmagawo osiyanasiyana monga: chakudya, ntchito zokopa alendo komaso anthu kulembedwa ntchito. Nsomba zimagwiritsidwa ntchito ngati ndiwo mmoyo watsikunditsiku ndikumathandizira thanzi laanthu. Pantchito zokopa alendo, nsomba ya mtundu wa Chambo imapezeka ku Malawi kokha kuno zimene zimabweretsa chikoka chachikulu ku mzika zamaiko ambiri kudzawona nsombayi. Ulimi wasomba kuti utheke pamafunika ogwira ntchito ochuluka posamalira, kudyetsera ndikupha nsombazi zikakula ndipo anthu amalembedwa ntchito ndikumathandizika pamoyo watsikunditsiku akalandira malipiro mwezi ukatha.
Kutengera mavuto omwe amakhalapo pa ulimiwu kuti munthu apange; ndizofunika kuti boma kudzera mu unduna wazaulimi komaso magulu ena okhudzidwa azithandizira alimi ochepekedwa kuti ulimiwu upite patsogolo mudziko muno. Ulimiwu ukapita patsogolo zidzathandizira pachitukuko chadziko lino, zamadyedwe komaso zachuma.



Comments
Post a Comment